< ᎨᏥᏅᏏᏛ ᏄᎾᏛᏁᎵᏙᎸᎢ 20 >

1 ᎤᏓᏑᏰᏛᏃ ᎠᎾᎵᏖᎸᎲᏍᎬ ᎤᎵᏙᎯᏍᏔᏅ, ᏉᎳ ᏫᏚᏯᏅᎲᎩ ᎠᏃᎯᏳᎲᏍᎩ, ᏚᏲᎵᎸᏃ, ᎤᏂᎩᏒᎩ ᏑᏏᏙᏂ ᎤᏪᏅᏍᏗᏱ ᎤᏰᎸᏅᎩ.
Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya.
2 ᎾᎿᎭᏃ ᎤᏪᏙᏅ ᎠᎴ ᎤᏣᏘ ᏚᏪᏁᏔᏅ, ᎠᏂᎪᎢ ᎤᎾᏤᎵᎪᎯ ᏭᎷᏨᎩ.
Iye anayendera madera a kumeneko, nalimbitsa mtima anthu, ndipo pomaliza pake anapita ku Grisi.
3 ᎾᎿᎭᏃ ᏦᎢ ᎢᏯᏅᏙ ᎤᏪᏙᎸ, ᎠᎴ ᎠᏂᏧᏏ ᏧᏄᎪᏔᏅ ᎪᎱᏍᏗ ᎬᏩᏁᏗᏱ, ᏏᎵᏱ ᏓᏰᏏᏒᎩ ᏥᏳᎯ ᏛᏣᏂᏒᎩ, ᎤᏓᏅᏖᎸᎩ ᏛᎤᏨᏍᏗᏱ ᎼᏏᏙᏂ ᏭᎶᎯᏍᏗᏱ.
Kumeneko anakhala miyezi itatu. Popeza kuti Ayuda anakonza zomuchita chiwembu pamene amati azinyamuka kupita ku Siriya pa sitima ya pamadzi, iye anaganiza zobwereranso kudzera ku Makedoniya.
4 ᎡᏏᏱᏃ ᎬᏗᏍᎩ ᎬᏩᏍᏓᏩᏛᏒᎩ ᏐᏇᏓ ᏈᎵᏱ ᎡᎯ, ᏕᏏᎶᏂᎦᏃ ᎠᏁᎯ ᎡᎵᏍᏓᎦ ᎠᎴ ᏏᎬᏓ, ᎦᏯᏃ ᏓᏈ ᎡᎯ, ᏗᎹᏗᏃ, ᎡᏏᏱᏃ ᎠᏁᎯ ᏗᎩᎦ ᎠᎴ ᏠᏆᎹ.
Iye anapita pamodzi ndi Sopatro mwana wa Puro wa ku Bereya, Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Derbe ndi Timoteyo, ndipo a ku Asiya anali Tukiko ndi Trofimo.
5 ᎾᏍᎩ ᎯᎠ ᎢᎬᏱ ᏄᏁᏅᏒᎩ ᏠᎠᏏ ᏓᎪᎩᏚᏘᏴᎩ.
Anthu amenewa anatsogola ndipo anakatidikira ku Trowa.
6 ᎾᎪᏔᏅᎾᏃ ᎦᏚ ᎠᎩᏍᏗᏱ ᎨᏒ ᎤᎶᏐᏅ, ᏈᎵᎩᏱ ᏥᏳᎯ ᎣᎦᏣᏅᎩ, ᎯᏍᎩᏃ ᏫᏄᏒᎸ ᏠᎠᏏ ᏫᏙᏥᏩᏛᎲᎩ; ᎾᎿᎭᏃ ᎦᎵᏉᎩ ᏧᏒᎯᏛ ᎣᎨᏙᎸᎩ.
Koma ife tinayenda pa sitima ya pamadzi kuchokera ku Filipi chitatha Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Patapita masiku asanu tinakumana nawo enawo ku Trowa, ndipo tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri.
7 ᎢᎬᏱᏱᏃ ᎢᎦ ᏑᎾᏙᏓᏆᏍᏗ ᎨᏒᎢ ᎦᏚ ᎠᎬᎭᎷᏯᏍᏗᏱ ᎤᎬᏩᎵ ᎠᏃᎯᏳᎲᏍᎩ ᎤᎾᏓᏟᏌᏅ, ᏉᎳ ᏚᎵᏥᏙᏁᎸᎩ, ᎤᎩᏨᏛᏉ ᎤᏪᏅᏍᏗ ᎨᏒᎢ; ᎠᎴ ᎡᏃᏱ ᎠᏰᎵ ᏫᎬᏩᏛᏅᎩ ᎦᏬᏂᏍᎬᎩ.
Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku.
8 ᎠᎴ ᎤᏣᏛᎩ ᏓᏨᏍᏛᎩ ᎦᎸᎳᏗ ᎾᎿᎭᏓᏂᎳᏫᎥᎢ.
Munali nyale zambiri mʼchipinda chammwamba mʼmene tinasonkhanamo.
9 ᎩᎶᏃ ᎢᏳᏍᏗ ᎠᏫᏄᏣ ᏳᏘᎦ ᏧᏙᎢᏛ ᎠᏦᎳᏅ ᎤᏬᎸᎩ, ᎠᏍᏓᏯ ᎦᎵᎲᎩ; ᏉᎳᏃ ᎪᎯᏗᏳ ᎠᎵᏥᏙᎲᏍᎬ ᎢᏳᏍᏗ, ᎦᎵᎲ ᎤᏪᏇᏴᏒᎩ ᎠᎴ ᏦᎢᏁ ᏗᏲᏓᏝᎲ ᏓᏳᏙᎣᏒᎩ, ᎠᎴ ᎠᏥᏁᏒᎩ ᎤᏲᎱᏒᎯ ᎨᏒᎩ.
Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa.
10 ᏉᎳᏃ ᎤᏠᎣᏒ ᎤᎵᏢᏅᎩ, ᎠᎴ ᎤᏄᎶᎸ ᎯᎠ ᏄᏪᏒᎩ; ᏞᏍᏗ ᏱᏣᏕᏯᏔᏁᎴᏍᏗ, ᎬᏅᏰᏃ ᎠᏏᏉ ᎠᏯᎠ.
Paulo anatsika, nadziponya pa mnyamatayo, namukumbatira. Paulo anati, “Musadandaule, ali moyo!”
11 ᏔᎵᏁᏃ ᎢᎤᎩᎳᏫᏒ, ᎠᎴ ᎤᎬᎭᎷᏴ ᎦᏚ, ᎠᎴ ᎤᎬ, ᎠᎴ ᎪᎯᏛ ᎤᏬᏂᏒ, ᎤᎩᏨᏕᏱ ᎬᏗᏍᎩ, ᎿᎭᏉ ᎤᏂᎩᏒᎩ.
Kenaka Paulo anakweranso, mʼchipinda muja nanyema buledi nadya. Atayankhula mpaka kucha, anachoka.
12 ᎤᎾᏘᎿᎭᏫᏛᎲᎩᏃ ᎠᏫᏄᏣ ᎬᏃᏛ, ᎠᎴ ᎥᏝ ᎤᏍᏗᏉ ᎣᏍᏛ ᏳᎾᏓᏅᏓᏕᎢ.
Anthu anatenga mnyamatayo kupita kwawo ali moyo ndipo anatonthozedwa mtima kwambiri.
13 ᎠᎴ ᎠᏴ ᎢᎬᏱ ᏃᎨᏅᏒᎩ ᏥᏳ ᏗᏔᎸᎢ, ᎠᎴ ᎣᎦᏣᏅ, ᎡᏐᏏ ᏬᎩᎶᏒᎩ; ᎾᎿᎭᏉᎳ ᎣᏥᏲᏗᏱ ᎣᎩᏰᎸᏒᎩ, ᎾᏍᎩᏰᏃ ᎢᏳᏪᏛ ᎨᏒᎩ, ᎤᏩᏒ ᎡᎳᏗᏉ ᏭᎶᎯᏍᏗᏱ ᎤᏰᎸᏒᎩ.
Ife tinatsogola kukakwera sitima ya pa madzi kupita ku Aso, kumene tinayembekeza kukatenga Paulo. Iye anakonza motero chifukwa amayenda wapansi.
14 ᎡᏐᏏᏃ ᎣᎩᏩᏛᎲ ᎣᏥᏴᏔᏅᎩ, ᎠᎴ ᎻᏗᎵᏂ ᏬᎩᎷᏨᎩ;
Pamene anakumana nafe ku Aso tinamutenga ndipo tinapita ku Mitilene.
15 ᎾᎿᎭᏃ ᏫᏱᎦᏣᏅ ᎤᎩᏨᏛ ᎦᏲᏏ ᏧᏳᎪᏗ ᎣᏥᏂᏒᎩ. ᎤᎩᏨᏛᏃ ᏎᎼᏏ ᏬᎩᎷᏨᎩ; ᏠᏥᎵᏯᏃ ᎣᎩᏒᎸ ᎤᎩᏨᏛ ᎹᎵᏔ ᏬᎩᎷᏨᎩ.
Mmawa mwake tinachoka kumeneko pa sitima ya pamadzi ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Tsiku linalo tinawolokera ku Samo, ndipo tsiku linanso tinafika ku Mileto.
16 ᏉᎳᏰᏃ ᏧᏭᎪᏔᏅᎯ ᎨᏒᎩ ᎤᎶᎯᏍᏗᏱᏉ ᎡᏈᏌ, ᏅᏓᎦᎵᏍᏙᏗᏍᎬᎩ ᏄᏚᎵᏍᎬᎾ ᎨᏒ ᎡᏏᏱ ᎤᏪᏓᏍᏗᏱ; ᎤᏩᏅᎬᎩᏰᏃ, ᎢᏳᏃ ᏰᎵ ᎾᏍᎩ ᎢᎬᏩᏛᏁᏗ ᏱᎩ, ᏥᎷᏏᎵᎻ ᏭᎷᎯᏍᏗᏱ ᎯᏍᎦᏍᎪᎯᏁ ᎢᎦ ᎠᏍᏆᎵᏍᎬᎢ.
Paulo anali atatsimikiza kuti alambalale Efeso kuopa kutaya nthawi ku Asiya, pakuti ankafulumira kuti akafike ku Yerusalemu kuti ngati nʼkotheka kuti tsiku la Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.
17 ᎹᎵᏔᏃ ᎤᏓᏅᏒᎩ ᎡᏈᏌ ᏫᏚᏯᏅᎲᎩ ᏗᎨᎦᏁᎶᏗ ᏧᎾᏁᎶᏗ ᎤᎾᏓᏡᎬᎢ.
Paulo ali ku Mileto, anatumiza mawu ku Efeso kuyitana akulu ampingo.
18 ᎬᏩᎷᏤᎸᏃ ᎯᎠ ᏂᏚᏪᏎᎸᎩ; ᎢᏥᎦᏔᎭ ᎢᎬᏱᏱ ᎢᎦ ᎡᏏᏱ ᏣᎩᎾᏄᎪᏥᎸᎩ ᏅᏓᎬᏩᏓᎴᏅᏛ, ᏄᏍᏛ ᎠᏆᎵᏂᏙᎸ ᎢᏤᎲ ᏂᎪᎯᎸᎢ.
Iwo atafika, Paulo anati, “Inu mukudziwa mmene ndinakhalira nanu nthawi yonse imene ndinali nanu kuyambira tsiku loyamba limene ndinafika ku Asiya.
19 ᏕᏥᎧᎿᎭᏩᏛᎡᎲ ᎤᎬᏫᏳᎯ ᏂᎦᎥ ᎪᎱᏍᏗ ᎾᏆᎵᏍᎦᏍᏛᎾ ᎨᏒᎢ, ᎠᎴ ᏕᏥᎦᏌᏬᎢᎲᎢ, ᎠᎴ ᎠᎩᎪᎵᏰᏍᎩ ᎠᏆᎵᏩᏛᎡᎲᎢ, ᏅᏗᎦᎵᏍᏙᏗᏍᎬ ᎠᏂᏧᏏ ᎪᎱᏍᏗ ᎬᏋᏁᏗᏱ ᏚᏄᎪᏔᏅᎢ.
Ndinatumikira Ambuye modzichepetsa kwambiri ndiponso ndi misozi, ngakhale ndinayesedwa kwambiri ndi ziwembu za Ayuda.
20 [ ᎠᎴ ᎢᏥᎦᏔᎭ ] ᎪᎱᏍᏗ ᎢᏣᎵᏍᏕᎸᏙᏗ ᎠᏋᏍᎦᎳᏅᎯ ᏂᎨᏒᎾ ᎨᏒᎢ, ᎢᏨᎾᏄᎪᏫᏎᎸᏉᏍᎩᏂ ᎠᎴ ᏕᏨᏰᏲᏅ ᏕᎦᎳᏫᎥᎢ ᎠᎴ ᏓᏓᏁᎳᏗᏒᎢ,
Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba.
21 ᎬᏂᎨᏒ ᏂᎦᏥᏴᏁᎲ ᎠᏂᏧᏏ ᎠᎴ ᎾᏍᏉ ᎠᏂᎪᎢ ᎾᏍᎩ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎦᏁᏟᏴᎡᏗ ᎨᏒ ᎣᏓᏅᏛᎢ, ᎠᎴ ᎪᎯᏳᏗ ᎨᏒ ᎤᎬᏫᏳᎯ ᎢᎦᏤᎵ ᏥᏌ ᎦᎶᏁᏛ.
Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu.
22 ᎿᎭᏉᏃ ᎬᏂᏳᏉ ᎠᏆᏓᏅᏛ ᎦᎸᎢᏛ ᏥᎷᏏᎵᎻ ᏫᏥᎦᏘ, ᏂᏥᎦᏔᎲᎾ ᏅᏗᏆᎵᏍᏓᏁᎵᏒ ᎾᎿᎭᏂ,
“Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.”
23 ᎦᎸᏉᏗᏳᏍᎩᏂᏃᏅ ᎠᏓᏅᏙ ᎬᏂᎨᏒ ᏂᎬᏁᎭ ᏕᎦᏚᏩᏗᏒᎢ, ᎾᏍᎩ ᎬᎩᎦᏘᏴ ᎥᏆᎸᏍᏗ ᎨᏒ ᎠᎴ ᎤᏲ ᎢᏯᏆᎵᏍᏓᏁᏗ ᎨᏒᎢ.
Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira.
24 ᎠᏎᏃ ᎾᏍᎩ ᎯᎠ ᏧᏓᎴᏅᏛ ᎥᏝ ᎪᎱᏍᏗ ᏯᎩᏖᎸᎲᏍᎦ, ᎠᎴ ᎾᏍᏉ ᎬᏅ ᎥᏝ ᎤᏣᏘ ᏯᎩᎸᏉᏗ, ᎢᏳᏃ ᎤᎵᎮᎵᏍᏗ ᏯᏆᏓᏅᏔ ᏯᎩᏍᏆᏛ ᎦᎴᏂᏙᎲᎢ, ᎠᎴ ᎤᎬᏫᏳᎯ ᏥᏌ ᎠᎩᏁᎸᎯ ᏗᎦᎸᏫᏍᏓᏁᏗ ᎨᏒᎢ, ᎬᏂᎨᏒ ᏂᎬᏁᎲ ᎣᏍᏛ ᎧᏃᎮᏛ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎬᏩᎦᏘᏯ ᎤᏓᏙᎵᏍᏗ ᎨᏒ ᎧᏃᎮᏍᎩ.
Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.
25 ᎿᎭᏉᏃ ᎬᏂᏳᏉ ᏥᎦᏔᎭ ᏂᎯ ᏂᏥᎥᎢ, ᎢᏨᏰᎳᏗᏙᎸᎯ ᎦᎵᏥᏙᎲᏍᎬ ᏥᏃᎮᏍᎬ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎤᏤᎵᎪᎯ, ᎠᏆᎧᏛ ᎿᎭᏉ ᎢᏥᎪᏩᏛᏗ ᏂᎨᏒᎾ ᎨᏒᎢ.
“Tsopano ndikudziwa kuti inu nonse amene ndinakuyenderani ndi kumakulalikirani ufumu wa Mulungu simudzaonanso nkhope yanga.
26 ᎾᏍᎩᏃ ᎢᏳᏍᏗ ᎪᎯ ᎢᎦ ᎢᏥᎦᏔᎯ ᏂᏨᏴᎦ, ᎩᎶ ᎤᏂᎩᎬ ᎾᏆᏓᏅᎦᎸᎾ ᎨᏒᎢ.
Chifukwa chake, ine ndikukuwuzani lero kuti ndilibe mlandu ndi munthu aliyense.
27 ᎥᏝᏰᏃ ᎠᎩᏍᎦᎸᎯ ᏱᎩ ᎬᏂᎨᏒ ᎢᏨᏴᏁᏗᏱ ᏂᎦᎥ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎤᏓᏅᏖᎸᎢ.
Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu.
28 ᎾᏍᎩ ᎢᏳᏍᏗ ᎢᏣᏓᎦᏌᏯᏍᏕᏍᏗ ᎢᏨᏒ, ᎠᎴ ᏕᏥᎦᏌᏯᏍᏕᏍᏗ ᏂᎦᏛ ᏑᎾᏓᏡᎩ ᎨᏒᎢ, ᎾᏍᎩ ᏗᏥᎦᏘᏯ ᎢᏨᏁᎸᎯ ᏥᎩ ᎦᎸᏉᏗᏳ ᎠᏓᏅᏙ, ᏗᏤᎳᏍᏗᏱ ᏧᎾᏁᎶᏗ ᎤᎾᏓᏡᎬ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᏧᏤᎵᎦ, ᎾᏍᎩ ᎤᏩᏒ ᎤᎩᎬ ᏧᎫᏴᏔᏅᎯ ᏥᎩ.
Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake.
29 ᎯᎠᏰᏃ ᎾᏍᎩ ᏥᎦᏔᎭ, ᎿᎭᏉ ᎠᎩᏁᎴᏍᏗ, ᎤᏂᎬᎥᏍᎩ ᏩᏯ ᏓᎨᏣᏓᏑᏴᏂ, ᏂᏓᏂᏙᎵᎬᎾ ᎨᏎᏍᏗ ᏑᎾᏓᏡᎩ ᎨᏒᎢ.
Ndikudziwa kuti ndikachoka ine, padzafika mimbulu yolusa pakati panu imene sidzalekerera gulu lankhosalo.
30 ᎠᎴ ᎾᏍᏉ ᎢᏨᏒ ᎢᏣᏓᏡᎬ ᏛᏂᎾᏄᎪᏥ ᎠᏂᏍᎦᏯ ᎤᏣᏘᏂ ᎾᏂᏪᏍᎨᏍᏗ ᎠᏂᏬᏂᏍᎨᏍᏗ, ᎠᏃᎯᏳᎲᏍᎩ ᏧᎾᏘᎿᎭᏫᏛᏗᏱ ᎤᏂᏰᎸᏎᏍᏗ.
Ngakhale pakati pa inu nokha padzapezeka anthu oyankhula zonama ndi cholinga chofuna kukhala ndi ophunzira kuti awatsate.
31 ᎾᏍᎩ ᎢᏳᏍᏗ ᎢᏥᏯᏫᏍᎨᏍᏗ, ᎠᎴ ᎢᏣᏅᏖᏍᏗ ᏦᎢ ᏧᏕᏘᏴᏛ ᏂᏥᏑᎵᎪᎬᎾ ᏒᏃᏱ ᎠᎴ ᎢᎦ ᏗᎦᏥᎦᏌᏬᎢᎯ ᎢᏥᏏᏴᏫᎭ ᎢᏨᏰᏯᏔᏅᎢ.
Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.
32 Ꭷ, ᎢᏓᏓᏅᏟ, ᎿᎭᏉ ᏕᏨᏲᎯ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎢᏥᏙᎵᏍᏗᏱ, ᎤᏮᏙᏗᏱ, ᎧᏃᎮᏛ ᎬᏩᎦᏘᏯ ᎤᏓᏙᎵᏍᏗ ᎨᏒ ᎧᏃᎮᏍᎩ, ᎾᏍᎩ ᏰᎵ ᎨᏣᏁᏍᎨᏗ ᏥᎩ, ᎠᎴ ᎢᏣᏤᎵ ᏰᎵ ᎢᎨᏨᏁᏗ ᏥᎩ ᎾᏍᎩ ᏂᎦᏛ ᎤᎾᏓᏅᏘ ᎢᎨᎬᏁᎸᎯ ᎤᎾᏤᎵ ᎢᏳᎵᏍᏙᏗ ᎨᏒᎢ.
“Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa.
33 ᎥᏝ ᎩᎶ ᏥᏯᏚᎸᎡᎸᎯ ᏱᎩ ᎠᏕᎸ ᎤᏁᎬ ᎠᎴ ᎠᏕᎸ ᏓᎶᏂᎨ ᎠᎴ ᏗᏄᏬ.
Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense.
34 ᎢᏨᏒᏰᏃ ᎢᏥᎦᏔᎭ ᎯᎠ ᎾᏍᎩ ᏗᏉᏰᏂ ᏓᏋᏔᏅᎯ ᎠᎩᏩᏛᎲ ᎠᎩᏂᎬᏎᎲ ᎠᏋᏒ ᎠᎴ ᎾᏍᏉ ᎣᏤᎯ.
Inu nomwe mukudziwa kuti manja angawa ananditumikira kuti tipeze zimene ine ndi anzanga tinkazifuna.
35 ᏂᎦᏛ ᎬᏂᎨᏒ ᏂᏨᏴᏁᎸ ᎾᏍᎩ ᎢᏣᏛᏁᏗᏱ ᏕᏥᎸᏫᏍᏓᏁᎲ ᏗᏥᏍᏕᎸᏗᏱ ᏗᏂᏩᎾᎦᎳᎢ, ᎠᎴ ᎢᏣᏅᏓᏗᏍᏗᏱ ᏧᏁᏤ ᎤᎬᏫᏳᎯ ᏥᏌ, ᎯᎠ ᏥᏄᏪᏎᎢ, “ᎤᏟ ᎣᏏᏳ ᎠᏓᏅᏓᏗᏍᏗ ᏴᏓᏁᎭ, ᎡᏍᎦᏉ ᏴᏓᏗᏁᎭ.”
Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’”
36 ᎾᏍᎩᏃ ᎯᎠ ᏄᏪᏒ, ᏚᎵᏂᏆᏅᏅᎩ ᎠᎴ ᏂᎦᏛ ᎠᏂᎦᏔᎲ ᎤᏓᏙᎵᏍᏔᏅᎩ.
Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera.
37 ᎾᎦᏛᏃ ᎤᏣᏘ ᏚᎾᏠᏱᎸᎩ, ᎠᎴ ᏉᎳ ᎠᎩᎵᎨᏂ ᎤᏂᏯᎸᏨ ᎬᏩᏔᏪᏙᏅᎩ.
Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona.
38 ᎤᏲ ᎤᏂᏰᎸᏒᎩ Ꮀ ᎤᎬᏫᏳᏒ ᏅᏓᎦᎵᏍᏙᏗᏍᎬ ᎤᏁᏨ ᎾᏍᎩ ᎤᎧᏛ ᎿᎭᏉ ᎤᏂᎪᏩᏛᏗ ᏂᎨᏒᎾ ᎨᏒᎢ. ᏥᏳᏃ ᏗᏔᎸᎢ ᏫᎬᏪᎧᏅᎩ.
Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.

< ᎨᏥᏅᏏᏛ ᏄᎾᏛᏁᎵᏙᎸᎢ 20 >