< 1 Atesalonika 1 >

1 Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. Chisomo ndi mtendere kwa inu.
Павел и Силуан и Тимофей церкви Солунстей о Бозе Отце и Господе Иисусе Христе: благодать вам и мир от Бога Отца нашего и Господа Иисуса Христа.
2 Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu.
Благодарим Бога всегда о всех вас, поминание о вас творяще в молитвах наших,
3 Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.
непрестанно поминающе ваше дело веры, и труд любве, и терпение упования Господа нашего Иисуса Христа, пред Богом и Отцем нашим,
4 Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani,
ведяще, братие возлюбленная, от Бога избрание ваше:
5 chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni.
яко благовествование наше не бысть к вам в слове точию, но и в силе, и в Дусе Святе, и во извещении мнозе, якоже и весте, какови быхом в вас ради вас.
6 Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.
И вы подобницы бысте нам и Господу, приемше слово в скорби мнозе с радостию Духа Святаго,
7 Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya.
яко быти вам образ всем верующым в Македонии и Ахаии.
8 Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu,
От вас бо промчеся слово Господне не токмо в Македонии и Ахаии, но и во всяко место вера ваша, яже к Богу, изыде, яко не требовати нам глаголати что.
9 pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona.
Тии бо о нас возвещают, каков вход имехом к вам, и како обратистеся к Богу от идол, работати Богу живу и истинну
10 Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera.
и ждати Сына Его с небес, Егоже воскреси из мертвых, Иисуса, избавляющаго нас от гнева грядущаго.

< 1 Atesalonika 1 >