< Yobu 25 >

1 Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, 2 “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako. 3 Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani? 4 Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro? 5 Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake, 6 nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!”

< Yobu 25 >