< Masalimo 47 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Ombani mʼmanja, inu anthu onse; fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe. 2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba; Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi! 3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu; anayika anthu pansi pa mapazi athu. 4 Iye anatisankhira cholowa chathu, chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda. (Sela) 5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe, Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga. 6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando; imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando. 7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi; imbirani Iye salimo la matamando. 8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu; Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera. 9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana monga anthu a Mulungu wa Abrahamu, pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu; Iye wakwezedwa kwakukulu.

< Masalimo 47 >