< Mark 8 >

1 In those days the multitude being very great, and having nothing to eat, Jesus called his disciples [unto him], and saith unto them,
Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo,
2 I have compassion on the multitude, because they have now been with me three days, and have nothing to eat:
“Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya.
3 And if I send them away fasting to their own houses, they will faint by the way: for divers of them came from far.
Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”
4 And his disciples answered him, From whence can a man satisfy these [men] with bread here in the wilderness?
Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”
5 And he asked them, How many loaves have ye? And they said, Seven.
Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
6 And he commanded the people to sit down on the ground: and he took the seven loaves, and gave thanks, and brake, and gave to his disciples to set before [them]; and they did set [them] before the people.
Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero.
7 And they had a few small fishes: and he blessed, and commanded to set them also before [them].
Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire.
8 So they did eat, and were filled: and they took up of the broken [meat] that was left seven baskets.
Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri.
9 And they that had eaten were about four thousand: and he sent them away.
Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo,
10 And straightway he entered into a ship with his disciples, and came into the parts of Dalmanutha.
analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.
11 And the Pharisees came forth, and began to question with him, seeking of him a sign from heaven, tempting him.
Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba.
12 And he sighed deeply in his spirit, and saith, Why doth this generation seek after a sign? verily I say unto you, There shall no sign be given unto this generation.
Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.”
13 And he left them, and entering into the ship again departed to the other side.
Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.
14 Now [the disciples] had forgotten to take bread, neither had they in the ship with them more than one loaf.
Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato.
15 And he charged them, saying, Take heed, beware of the leaven of the Pharisees, and [of] the leaven of Herod.
Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”
16 And they reasoned among themselves, saying, [It is] because we have no bread.
Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”
17 And when Jesus knew [it], he saith unto them, Why reason ye, because ye have no bread? perceive ye not yet, neither understand? have ye your heart yet hardened?
Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa?
18 Having eyes, see ye not? and having ears, hear ye not? and do ye not remember?
Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira?
19 When I brake the five loaves among five thousand, how many baskets full of fragments took ye up? They say unto him, Twelve.
Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?” Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”
20 And when the seven among four thousand, how many baskets full of fragments took ye up? And they said, Seven.
“Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?” Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
21 And he said unto them, How is it that ye do not understand?
Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”
22 And he cometh to Bethsaida; and they bring a blind man unto him, and besought him to touch him.
Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze.
23 And he took the blind man by the hand, and led him out of the town; and when he had spit on his eyes, and put his hands upon him, he asked him if he saw ought.
Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”
24 And he looked up, and said, I see men as trees, walking.
Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”
25 After that he put [his] hands again upon his eyes, and made him look up: and he was restored, and saw every man clearly.
Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino.
26 And he sent him away to his house, saying, Neither go into the town, nor tell [it] to any in the town.
Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”
27 And Jesus went out, and his disciples, into the towns of Cæsarea Philippi: and by the way he asked his disciples, saying unto them, Whom do men say that I am?
Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”
28 And they answered, John the Baptist: but some [say], Elias; and others, One of the prophets.
Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”
29 And he saith unto them, But whom say ye that I am? And Peter answereth and saith unto him, Thou art the Christ.
Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?” Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”
30 And he charged them that they should tell no man of him.
Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.
31 And he began to teach them, that the Son of man must suffer many things, and be rejected of the elders, and [of] the chief priests, and scribes, and be killed, and after three days rise again.
Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.”
32 And he spake that saying openly. And Peter took him, and began to rebuke him.
Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
33 But when he had turned about and looked on his disciples, he rebuked Peter, saying, Get thee behind me, Satan: for thou savourest not the things that be of God, but the things that be of men.
Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
34 And when he had called the people [unto him] with his disciples also, he said unto them, Whosoever will come after me, let him deny himself, and take up his cross, and follow me.
Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata.
35 For whosoever will save his life shall lose it; but whosoever shall lose his life for my sake and the gospel’s, the same shall save it.
Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa.
36 For what shall it profit a man, if he shall gain the whole world, and lose his own soul?
Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake?
37 Or what shall a man give in exchange for his soul?
Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake?
38 Whosoever therefore shall be ashamed of me and of my words in this adulterous and sinful generation; of him also shall the Son of man be ashamed, when he cometh in the glory of his Father with the holy angels.
Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”

< Mark 8 >