< יחזקאל 33 >

ויהי דבר יהוה אלי לאמר 1
Yehova anandiyankhula nati:
בן אדם דבר אל בני עמך ואמרת אליהם ארץ כי אביא עליה חרב ולקחו עם הארץ איש אחד מקציהם ונתנו אתו להם לצפה 2
“Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda.
וראה את החרב באה על הארץ ותקע בשופר והזהיר את העם 3
Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo.
ושמע השמע את קול השופר ולא נזהר ותבוא חרב ותקחהו--דמו בראשו יהיה 4
Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha.
את קול השופר שמע ולא נזהר דמו בו יהיה והוא נזהר נפשו מלט 5
Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka.
והצפה כי יראה את החרב באה ולא תקע בשופר והעם לא נזהר ותבוא חרב ותקח מהם נפש--הוא בעונו נלקח ודמו מיד הצפה אדרש 6
Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’
ואתה בן אדם צפה נתתיך לבית ישראל ושמעת מפי דבר והזהרת אתם ממני 7
“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze.
באמרי לרשע רשע מות תמות ולא דברת להזהיר רשע מדרכו--הוא רשע בעונו ימות ודמו מידך אבקש 8
Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake.
ואתה כי הזהרת רשע מדרכו לשוב ממנה ולא שב מדרכו--הוא בעונו ימות ואתה נפשך הצלת 9
Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
ואתה בן אדם אמר אל בית ישראל כן אמרתם לאמר כי פשעינו וחטאתינו עלינו ובם אנחנו נמקים ואיך נחיה 10
“Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’”
אמר אליהם חי אני נאם אדני יהוה אם אחפץ במות הרשע כי אם בשוב רשע מדרכו וחיה שובו שובו מדרכיכם הרעים ולמה תמותו--בית ישראל 11
Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?
ואתה בן אדם אמר אל בני עמך צדקת הצדיק לא תצילנו ביום פשעו ורשעת הרשע לא יכשל בה ביום שובו מרשעו וצדיק לא יוכל לחיות בה--ביום חטאתו 12
“Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’
באמרי לצדיק חיה יחיה והוא בטח על צדקתו ועשה עול--כל צדקתו לא תזכרנה ובעולו אשר עשה בו ימות 13
Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake.
ובאמרי לרשע מות תמות ושב מחטאתו ועשה משפט וצדקה 14
Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna,
חבל ישיב רשע גזלה ישלם בחקות החיים הלך לבלתי עשות עול--חיו יחיה לא ימות 15
monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa.
כל חטאתו אשר חטא לא תזכרנה לו משפט וצדקה עשה חיו יחיה 16
Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.
ואמרו בני עמך לא יתכן דרך אדני והמה דרכם לא יתכן 17
“Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama.
בשוב צדיק מצדקתו ועשה עול--ומת בהם 18
Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo.
ובשוב רשע מרשעתו ועשה משפט וצדקה--עליהם הוא יחיה 19
Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo.
ואמרתם לא יתכן דרך אדני איש כדרכיו אשפוט אתכם בית ישראל 20
Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.”
ויהי בשתי עשרה שנה בעשרי בחמשה לחדש--לגלותנו בא אלי הפליט מירושלם לאמר הכתה העיר 21
Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!”
ויד יהוה היתה אלי בערב לפני בוא הפליט ויפתח את פי עד בוא אלי בבקר ויפתח פי ולא נאלמתי עוד 22
Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.
ויהי דבר יהוה אלי לאמר 23
Ndipo Yehova anandiyankhula kuti:
בן אדם ישבי החרבות האלה על אדמת ישראל אמרים לאמר אחד היה אברהם ויירש את הארץ ואנחנו רבים לנו נתנה הארץ למורשה 24
“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’
לכן אמר אלהם כה אמר אדני יהוה על הדם תאכלו ועינכם תשאו אל גלוליכם--ודם תשפכו והארץ תירשו 25
Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli?
עמדתם על חרבכם עשיתן תועבה ואיש את אשת רעהו טמאתם והארץ תירשו 26
Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’
כה תאמר אלהם כה אמר אדני יהוה חי אני אם לא אשר בחרבות בחרב יפלו ואשר על פני השדה לחיה נתתיו לאכלו ואשר במצדות ובמערות בדבר ימותו 27
“Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri.
ונתתי את הארץ שממה ומשמה ונשבת גאון עזה ושממו הרי ישראל מאין עובר 28
Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako.
וידעו כי אני יהוה בתתי את הארץ שממה ומשמה על כל תועבתם אשר עשו 29
Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’
ואתה בן אדם--בני עמך הנדברים בך אצל הקירות ובפתחי הבתים ודבר חד את אחד איש את אחיו לאמר באו נא ושמעו מה הדבר היוצא מאת יהוה 30
“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’
ויבואו אליך כמבוא עם וישבו לפניך עמי ושמעו את דבריך ואותם לא יעשו כי עגבים בפיהם המה עשים אחרי בצעם לבם הלך 31
Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo.
והנך להם כשיר עגבים יפה קול ומטב נגן ושמעו את דבריך ועשים אינם אותם 32
Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.
ובבאה הנה באה--וידעו כי נביא היה בתוכם 33
“Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”

< יחזקאל 33 >